CryptApp

ULIMI WA NKHUKU

 

ULIMI WA NKHUKU

  • Ulimi wankhuku umakhudzana ndi ziweto monga nkhuku, abakha, nkhanga, nkhuku ndembo, nkhunda ndi zinziri.
  • Koma ulangizi uwu ukukamba za nkhuku
  • Mlimi amaweta nkhuku ndi zolinga izi: kupeza mazira ndi nyama komanso ndalama pa zifukwa izi nkhuku zimagawidwa m’magulu molingana ndi zomwe zimapereka.

Ubwino oweta Nkhuku

  • Zimakula mwachangu kuyerekeza ndi ziweto zina ngati mbuzi kapena ng’ombe.
  • Zimatipatsa ndiwo mosavuta (mazira ndi nyama)
  • Zimatipatsa manyowa
  • Timapeza ndalama tikagulitsa nkhuku kapena mazira
  • Sizisankhidwa kapena kusalidwa kumitundu komanso zipembedzo
  • Sizivuta kuweta kuyerekeza ndi ziweto zina.
  • Sizifuna malo ambiri kusiyana ndi ziweto zina.
Share this Doc
CONTENTS