CryptApp

ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE KA NKHUKU

ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE KA NKHUKU

 • Nkhuku zamakolo zimadzipezera chakudya zokha tikatsegulira
 • Zipatseni zakudya zowonjezera m’mawa ndi madzulo monga madeya, chimanga, zakudya zotsalira kukhitchini, ndiwo za masamba, ndi zakudya zopanga nokha kuti nkhuku zikule mwa thanzi.
 • Zidyetseni zikhokhombe za mazira zopera kuti zidzaikire mazira azikhokhombe zolimba.
 • Pangani chakudya cha nkhuku nokha posakaniza zinthu izi:
 • Magawo awiri a mgaiwa kapena madeya a chimanga
 • Gawo limodzi la ufa wa soya wokazinga ndi
 • kamchere pang’ono.
 • Sungani anapiye m’khola (basket layering) kuti azipatsidwa chakudya chokwanira ndichoyenera, komanso kuti anapiye akule bwino ndi kutetezeka kuzirombo monga a khwangwala ndi mbalame zina.

 • Zipatseni madzi abwino nkhuku nthawi zonse

Chomwera madzi

 • Kuti mudziwe zambiri za zakudya ndi kadyetsedwe ka nkhuku kafunseni kwa alangiza a ziweto m’dera lanu

Kuti nkhuku zanu zikhale ndi thanzi tsatirani izi:

 • Samalirani ndi kudyetsera bwino nkhuku zanu
 • Zipatseni katemera wa Lasota pa miyezi itatu ili yonse kapena I2 pa miyezi inayi iliyonse kuti muteteze nkhuku kumatenda a chitopa

 • Musapereke katemera kunkhuku zomwe zikudwala
 • Zimwetseni nkhuku mankhwala wopha njoka za m’mimba makamaka miyezi yapakati pa Disembala ndi Malichi pamene mvula ikugwa kuti nkhuku zikule ndi thanzi
 • Tenthani kapena kwilirani nkhuku zonse zimene zafa ndi matenda kuopetsa kufala kwa matendawo.
Share this Doc
CONTENTS