CryptApp

MAKOLA ANKHUKU

MAKOLA ANKHUKU

Makola ankhuku za makolo alipo a mitundu iwiri omwe ndi:

Lam’mwamba

Iri limamangidwa ndi zipangizo zopezeka mosabvuta monga nsungwi, bango

Khola likhale pa mlingo wa 1.0m kuchokera pansi

Lapansi

  • Mangani khola molingana ndi kuchuluka kwa nkhuku zanu, mwachitsanzo nkhuku 10 mpaka 15 zimafunika khola lotalika mita imodzi mbali zonse
  • Folerani denga la khola ndi udzu kapena malata kuti m’khola muzikhala mouma nthawi zonse
  • Ikani utuchi m’khola kuti nkhuku zizigona pabwino
  • Konzani malo abwino oyikira nkhuku kuti mazira asasweke komanso azikhala aukhondo
  • Onetsetsani kuti m’khola ndi mwaukhondo nthawi zonse.
Share this Doc
CONTENTS