CryptApp

NKHUKU ZA MAKOLO

NKHUKU ZA MAKOLO

Kusankha nkhuku zoweta

  • Sankhani nkhuku zimene zimakula msanga, zazikuluzikulu, zoswa kwambiri komanso zolera bwino anapiye

Kukwatitsa nkhuku za makolo ndi za Mikolongwe

  • Kwatitsani nkhuku za makolo ndi tambala wa Mikologwe kuti zikhale zokula mwamsanga, zoyikira mazira ambiri ndi kupereka nyama yochuluka
  • Tambala mmodzi mpatseni nkhuku zazikazi khumi (10)

Kusankha mazira oyenera kufungatira

  • Sungani mazira pamalo ouma, aukhondo, opanda fungo lina liri lonse kuti mazira asaonongeke
  • Onetsetsani kuti mazira oyenera kufungatira asapitilire masiku 10 kuchokera tsiku limene nkhuku zayikira
  • Sankhani mazira opanda chilema
  • Sakhani mazira akuluakulu

  • Lembani tsiku lomwe dzira laikiridwa padzira kuti mudziwe lomwe lakhalitsa
  • Chotsani mazira amene akhala nthawi yaitali, kuti nkhuku ikhalire okhawo amene sanapitirire masiku khumi (10) ataikiridwa

Share this Doc
CONTENTS